Judges 20:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye ife tsopano tikuti mubwere nawo anthuwo, anthu achabechabe aja a ku Gibea, kuti tiŵaphe, kuti potero tichotse kulaulaku m'dziko la Israele.” Koma Abenjamini sadafune kumva mau a Aisraele, abale ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pake, okhala m'Gibea, kuti tiwaphe, ndi kuchotsera Israele choipachi. Koma Benjamini sanafune kumvera mau a abale ao, ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono tikuti mutipatse anthu achabechabe a ku Gibeya kuti tiwaphe kuti tichotse chinthu choyipachi mʼdziko la Israeli.” Koma fuko la Benjamini silinafune kumvera zimene ananena Aisraeli anzawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pace, okhala m'Gibeya, kuti tiwaphe, ndi kucotsera Israyeli coipaci. Koma Benjamini sanafuna kumvera mau a abale ao, ana a Israyeli.