Judges 20:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adanyamuka napita ku Betele kukafunsa kwa Mulungu kuti, “Ndani mwa ife amene ayambe kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini?” Chauta adayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo limene liyambe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nauka ana a Israele, nakwera kunka ku Betele, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Aisraeli ananyamuka kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu. Iwo anati, “Ndani mwa ife amene angayambe kukamenyana ndi fuko la Benjamini?” Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nauka ana a Israyeli, nakwera kumka ku Beteli, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.