Judges 20:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraelewo adapita kukalira pamaso pa Chauta mpaka madzulo. Adakafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kachiŵiri kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu?” Chauta adayankha kuti, “Inde pitani mukamenyane nawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anapita kukalira pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana ndi a fuko la Benjamini abale athu?” Yehova anayankha kuti, “Pitani mukalimbane nawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.