Judges 20:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abenjamini adatulukanso mu mzinda wa Gibea, kukalimbana nawo tsiku lachiŵirilo, ndipo adapha ankhondo a Aisraele 18,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Benjamini anawatulukira ku Gibea m'mawa mwake, naononganso a ana a Israele amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachiwiri lomwelo Abenjamini anatulukanso mu mzinda wa Gibeya ndipo anaphanso ankhondo 18,000. Onse amene anawaphawo anali odziwa kugwiritsa ntchito bwino malupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Benjamini anawaturukira ku Gibeya m'mawa mwace, naononganso a ana a Israyeli amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.