Judges 20:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Aisraeli onse, gulu lonse la ankhondo, anapita ku Beteli kukalira pamaso pa Yehova. Anakhala pansi nasala zakudya tsiku lonse mpaka madzulo. Anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ana onse a Israyeli ndi anthu onse anakwera nafika ku Beteli, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.