Judges 20:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye ankayang'anira bokosilo masiku amenewo. Choncho Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu, kapena tingoleka?” Chauta adayankha kuti, “Pitaninso, pakuti maŵa ndidzaŵapereka m'manja mwanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Finehasi mwana wa Eliezara mwana wa Aaroni ndiye ankatumikira nthawi imeneyo. Tsono Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukachita nkhondo ndi mʼbale athu Abenjamini, kapena ayi?” Yehova anayankha kuti, “Pitaninso chifukwa mawa ndidzawapereka mʼmanja mwanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
namaima ku likasalo Pinehasi mwana wa Eleazare mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditurukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.