Judges 20:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abenjamini nawonso adatuluka kukamenyana nawo anthuwo, napita chapatali ndithu ndi mzindawo. Ndipo monga mwa masiku onse, adayamba kuŵamenya koopsa ndi kupha Aisraele makumi atatu amene anali m'miseu yaikulu, ena mu mseu waukulu wa ku Betele, ena mu mseu waukulu wa ku Gibea ndiponso ena kwina koyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natuluka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mudzi, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu amuna a Israele, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kunka ku Betele, ndi lina ku Gibea kuthengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abenjamini anatuluka kukamenyana nawo anthuwo ndipo anapita kutali ndi mzindawo. Iwo anayamba kupha Aisraeli monga poyamba paja, kotero kuti anapha anthu pafupifupi makumi atatu. Mitembo ya ena inali mu misewu yayikulu yopita ku Beteli ndi ku Gibeya, ndipo ina inali kwina poyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturuka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mudzi, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu amuna a Israyeli, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kumka ku Beteli, ndi lina ku Gibeya kuthengo.