Judges 20:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele osankhidwa amene adabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibea analipo 10,000, ndipo nkhondo idalimba kumeneko. Koma Abenjamini sankadziŵa kuti zoopsa zili pafupi kuŵagwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza pandunji pa Gibea amuna osankhika m'Israele monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwe kuti choipa chili pafupi kuwakhudza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli osankhidwa 10,000 ndiwo anabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibeya. Nkhondoyo inafika poyipa kwambiri mwakuti Abenjamini samadziwa kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza pandunji pa Gibeya amuna osankhika m'Israyeli monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwa kuti coipa ciri pafupi kuwakhudza.