Judges 20:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Abenjamini adaona kuti agonjetsedwa. Paja gulu lalikulu la Aisraele lidaathaŵa Abenjamini chifukwa linkadalira anthu aja amene lidaaŵaika kuti abisalire mzinda wa Gibea.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israele anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibea.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Abenjamini anaona kuti agonjetsedwa. Paja Aisraeli anathawa fuko la Benjamini chifukwa ankadalira anthu amene anawayika kuti abisalire mzinda wa Gibeya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israyeli anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibeya.