Judges 20:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu obisalira aja adafulumira kuuthira nkhondo mzinda wa Gibeawo. Adapha anthu onse amumzindamo ndi lupanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nafulumira olalirawo nathamangira Gibea, nabalalika olalirawo, nakantha mudzi wonse ndi lupanga lakuthwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anthu amene anabisala aja anachita changu kuwuthira nkhondo mzinda wa Gibeyawo. Ndipo anapha anthu onse a mu mzindawo ndi lupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nafulumira olalirawo nathamangira Gibeya, nabalalika olalirawo, nakantha mudzi wonse ndi lupanga lakuthwa.