Judges 20:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ambiriwo abwerere kudzamenya nkhondo. M'menemo nkuti Abenjamini atayamba kuŵamenya Aisraelewo koopsa ndi kupha anthu makumi atatu. Iwo ankati, “Ndithu, taŵapha monga poyamba paja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi nkhondo ya Israele inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israele, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiye kuti Aisraeli enawo abwerere ku nkhondo. Pa nthawiyo nʼkuti Abenjamini atayamba kale kumenya Aisraeliwo kwambiri ndi kupha pafupifupi anthu makumi atatu. Ndipo iwo ankanena kuti, “Ndithu tawapha monga poyamba paja.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi nkhondo ya Israyeli inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israyeli, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu Tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo.