Judges 20:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene utsi wachizindikiro uja udayamba kuti tolotolo kukwera kumwamba mumzindamo, Abenjamini adayang'ana kumbuyo, nkuwona mu mzinda wonsewo utsi uli tolotolo kukwera kumwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mudzi ngati utsi uli tolo, Abenjamini anacheuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene utsi wa chizindikiro uja unayamba kukwera tolotolo mmwamba kuchoka mu mzindamo, Abenjamini anayangʼana mʼmbuyo ndipo anangoona utsi mu mzinda onse uli tolotolo kukwera mmwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mudzi ngati utsi uti tolo, Abenjamini anaceuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba.