Judges 20:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵazinga Abenjaminiwo naŵapirikitsa ndi kuŵaonongeratu osaŵachitira chifundo mpaka ku dera la Gibea kuvuma kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anawazinga Abenjamini, anawapirikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibea, kotulukira dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawazungulira Abenjaminiwo, nawathamangitsa ndi kuwagonjetseratu osawachitira chifundo mpaka ku dera la kummawa kwa Gibeya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anawazinga Abenjamini, anawapitikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibeya, koturukira dzuwa.