Judges 20:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene adatsalira, adatembenuka nathaŵira ku dondo ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowo anthu 5,000 adaphedwa m'miseu yaikulu. Adaŵapirikitsabe Abenjaminiwo mkaka ku Gidomu, naphanso enanso 2,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natembenuka iwo, nathawira kuchipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m'makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ena anatembenuka nathawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowa Aisraeli anapha Abenjamini 5,000 mʼmisewu yayikulu. Anawapitikitsabe Abenjaminiwo mpaka kufika ku Gidomu ndi kuphanso ena 2,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natembenuka iwo, nathawira kucipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m'makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri.