Judges 20:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele adabwerera m'mbuyo kukamenyana ndi Abenjamini otsala, naŵapha ndi lupanga, anthu ndi nyama zomwe, pamodzi ndi zonse zimene adakumana nazo. Ndipo adatentha mizinda yonse imene adaipeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amuna a Israele anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m'mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anabwerera kukamenyana ndi Abenjamini otsala ndi kuwapha ndi lupanga kuphatikizapo ziweto ndi zonse anali nazo. Ndipo anayatsa moto mizinda yonse anayipeza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amuna a Israyeli anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m'mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza.