Judges 20:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Gibea adandiwukira nazinga nyumba imene munali ine nthaŵi ya usiku. Ankafuna kundipha ndipo adamchita zoipa mzikazi wangayo mwakhakhamizo mpaka iye adafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nandiukira eni ake a Gibea, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namchitira choipa mkazi wanga wamng'ono, nafa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usiku anthu a ku Gibeya anandiwukira, nazinga nyumba munali ine. Ankafuna kundipha ndipo anagona ndi mzikazi wanga momukakamiza mpaka anafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nandiukira eni ace a Gibeya, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namcitira coipa mkazi wanga wamng'ono, nafa iye,