Judges 21:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mpingo udatumiza kumeneko anthu 12,000 mwa anthu ao, olimba kwambiri, naŵalamula kuti, “Pitani mukaŵaphe anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndi lupanga. Mukaphenso akazi ndi ana omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala m'Yabesi-Giliyadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana ang'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho msonkhano unatumiza anthu ankhondo 12,000 ndi kuwalamula kuti, “Mukaphe anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi, kuphatikizapo akazi ndi ana.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala m'Yabesi-gileadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana ang'ono.