Judges 21:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati pa anthu a ku Yabesi-Giliyadi adapeza anamwali 400 amene sadadziŵepo amuna. Amenewo adabwera nawo ku zithando ku Silo, mzinda umene uli m'dziko la Kanani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapeza atsikana 400 pakati pa anthu okhala mu Yabesi Giliyadi amene anali asanadziwepo mwamuna ndipo anabwera nawo ku misasa ku Silo mʼdziko la Kanaani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-gileadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.