Judges 21:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adaŵamvera chifundo Abenjaminiwo chifukwa chakuti Chauta anali atachotsako anthu ena mu fuko limodzi la Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anamva chifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mafuko a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anamvera chisoni Abenjamini, chifukwa Yehova anachita ngati waligwerula dzino fuko la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anamva cifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mapfuko a Israyeli.