Judges 21:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono akuluakulu a mpingo adati, “Kodi tikaŵapezera kuti akazi anthu amene atsaliraŵa, popeza kuti akazi a fuko la Benjamini adaphedwa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo akulu a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho akuluakulu a msonkhano anati, “Kodi tikawapezera kuti akazi anthu otsalirawa kuti awakwatire popeza kuti akazi a fuko la Benjamini anaphedwa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo akuru a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini?