Judges 21:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adati, “Paja kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Chauta ku mzinda wa Silo.” Silo ali kumpoto kwa Betele, kuvuma kwa Lebona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iwo, Taonani, pali madyerero a Yehova chaka ndi chaka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Betele, kum'mawa kwa mseu wokwera kuchokera ku Betele kunka ku Sekemu, ndi kumwera kwa Lebona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anati, ‘Paja ku Silo kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Yehova. Tsono Silo ali kumpoto kwa Beteli, kummawa kwa msewu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kummwera kwa Lebona.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natiiwo, Taonani, pali madyerero a Yehova caka ndi caka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Beteli, kum'mawa kwa mseu wokwera kucokera ku Beteli kumka ku Sekemu, ndi kumwela kwa Lebona.