Judges 21:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adafika ku Betele, nakhala pansi kumeneko pamaso pa Mulungu mpaka madzulo, ndipo adafuula nalira ndi chisoni chambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anapita ku Beteli kumene anakakhala pansi pamaso pa Mulungu mpaka madzulo. Iwo anakweza mawu nalira kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anadza ku Beteli, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.