Judges 21:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene azibambo kapena alongo ao adzabwere kuno kudzadandaula, ife tidzaŵauza kuti, ‘Chonde, tiloleni kuti tiŵatenge, popeza kuti anthuŵa sitidaŵapezere akazi pomenya nkhondo, ndipo inunso simudachita kuŵapatsa akaziwo. Mukadatero bwenzi tsopano mutapalamula.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkha awa; mukadatero mukadapalamula tsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati abambo awo kapena alongo awo adzabwera kudzadandaula kwa ife, tidzawawuza kuti, ‘Chonde, tikomereni mtima powalola kuti atenga ana anu aakaziwo popeza kuti ife sitinawapezere akazi pomenya nkhondo. Inunso simunachite kuwapatsa. Mukanatero ndiye mukanapalamula.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wace kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkha awa; mukadatero mukadaparamula tsopano.