Judges 21:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abenjaminiwo adachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja adatengapo ao, molingana ndi chiŵerengero chao, napita nawo. Kenaka adanyamuka kubwerera ku dziko lakwao nakamanganso mizinda yatsopano ndi kumakhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachita chotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a ovina aja, amene anawatenga mwachifwamba; namuka iwo nabwerera ku cholowa chao, namanga midzi, nakhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abenjamini anachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja anagwirapo ena, malingana ndi chiwerengero chawo, nawatenga kuti akhale akazi awo. Kenaka ananyamuka kubwerera ku dziko la kwawo, nakamanganso mizinda yawo ndi kumakhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacita cotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a obvina aja, amene anawatenga mwacifwamba; namuka iwo nabwerera ku colowa cao, namanga midzi, nakhalamo.