Judges 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo ankati, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani zimenezi zachitika m'dziko la Aisraele, kuti lero fuko la Benjamini lilipafupi kuchotsedwa m'dziko la Israele?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israele, chachitika ichi chifukwa ninji m'Israele, kuti lasowa lero fuko limodzi m'Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ankanena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli, nʼchifukwa chiyani izi zachitika mʼdziko la Israeli kuti lero fuko limodzi lisowe mu Israeli?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israyeli, cacitika ici cifukwa ninji m'Israyeli kuti lasowa lero pfuko limodzi m'Israyeli?