Judges 21:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adati, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Aisraele amene sadafike ku msonkhano wa Chauta?” Paja anali atachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene sadapite kwa Chauta ku Mizipa kuti, “Munthu wotero ayenera kuphedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati ana a Israele, Ndani iye mwa mafuko onse a Israele amene sanakwere kudza kumsonkhano kwa Yehova? Pakuti panali lumbiro lalikulu pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Aisraeli anafunsa kuti, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Israeli sanafike ku msonkhano wa Yehova?” Anatero chifukwa anachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene alephere kupita ku Mizipa ndi kuti woteroyo ayenera kuphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati ana a Israyeli, Ndani iye mwa mapfuko onse a Israyeli amene sanakwera kudza kumsonkhano kwa Yehova? pakuti panali lumbiro lalikuru pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.