Judges 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta. Ndiye Chauta adapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kuti alimbane ndi Aisraele, chifukwa chakuti iwowo adaachita zinthu zoipira Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Tsono Yehova anapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya Mowabu kuti alimbane ndi Aisraeli aja popeza anachita zinthu zoyipira Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ana a Israyeli anaonjezanso kucita coipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Moabu pa Israyeli, popeza anacita coipa pamaso pa Yehova.