Judges 3:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa. Iyeyu anali Ehudi, mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini, munthu wamanzere. Aisraele ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kudzera kwa Ehudi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israele anatumiza mtulo m'dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Mowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli analiranso kwa Yehova, ndipo Iye anawawutsira mpulumutsi, Ehudi. Iyeyu anali mwana wa Gera, munthu wamanzere, wa fuko la Benjamini. Aisraeli ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, kudzera kwa Ehudi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israyeli anatumiza mtulo m'dzanja lace Ikwa Egiloni mfumu ya Moabu.