Judges 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iyeyo adabwerera pa malo a miyala yozokotedwa ku Giligala, ndipo atafika kwa mfumu adati, “Zikomo amfumu, ndimati ndikuuzeni mau achinsinsi.” Pamenepo mfumuyo idalamula atumiki ake kuti akhale chete, niŵatulutsa onsewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndili nao mau achinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani chete. Ndipo anatuluka onse akuimapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.” Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndiri nao mau acinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani cete. Ndipo anaturuka onse akuimapo.