Judges 3:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adadikira nthaŵi yaitali, kotero kuti sadaone konse chochita. Koma ataona kuti mfumuyo sidatsekulebe zitseko zija, adatenga kii natsekula zitsekozo, ndipo adangoona mfumu yao ili thasa pansi, itafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analindirira mpaka anachita manyazi; koma taonani, sanatsegule pamakomo pa chipinda chosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anadikira nthawi yayitali koma popanda chochitika. Koma ataona kuti mfumuyo sikutsekulabe zitseko za chipindacho, iwo anatenga makiyi ndi kutsekula zitsekozo, ndipo anangoona mbuye wawo atagwera pansi, ali wakufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analindirira mpaka anacita manyazi; koma taonani, sanatsegula pamakomo pa cipinda cosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa.