Judges 3:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza anthuwo kuti, “Tiyeni kuno, Chauta wapereka Amowabu, adani anu, m'manja mwanu.” Choncho anthuwo adamtsata nakalanda madooko a Yordani natsekereza Amowabuwo, osalola kuti munthu ndi mmodzi yemwe aoloke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amowabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amowabu madooko a Yordani, osalola mmodzi aoloke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amoabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amoabu madooko a Yordano, osalola mmodzi aoloke.