Judges 3:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo adapha Amowabu pafupi 10,000. Anthu onse ophedwawo anali amphamvu ndiponso odziŵa kumenya nkhondo, koma sadapulumukepo ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakantha Amowabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuke ndi mmodzi yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000. Ophedwawo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anathawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakantha Amoabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuka ndi mmodzi yense.