Judges 4:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Debora adauza Baraki kuti, “Dzukani, ndi lero tsiku limene Chauta wapereka Sisera m'manja mwanu. Kodi suja Chauta wakutsogolerani kale?” Pamenepo Baraki adatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumtsata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanaturuka kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika ku phiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.