Judges 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adasokoneza Sisera ndi magaleta ake onse, pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi ankhondo ake ankaŵatsata pambuyo alikupha anthu ambiri. Sisera adatsika pa galeta lake nayambapo kuthaŵa pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ambuye anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anasokoneza Sisera ndi magaleta ake pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi anthu ake anawapirikitsa ndipo Sisera anatsika pa galeta yake nayamba kuthawa pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ambuye anaononga Sisera, ndi magareta onse ndi gulu lankhondo lonse, adi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagareta nathawa coyenda pansi.