Judges 4:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Sisera adathaŵa pansi mpaka kukafika ku hema la Yaele, mkazi wa Hebere, Mkeni uja, pakuti panali mtendere pakati pa Yabini, mfumu ya ku Hazori, ndi banja la Hebere Mkeniyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe Sisera anathawa pansi mpaka anakafika ku tenti ya Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni uja, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori ndi banja la Heberi, Mkeni uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Sisera anathawira coyenda pansi ku hema wa Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Heberi Mkeni.