Judges 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanani, amene ankalamulira ku Hazori. Mtsogoleri wa ankhondo ake anali Sisera amene ankakhala ku Haroseti-Goimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wocita ufumu ku Hazori; kazembe wace wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.