Judges 4:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yaele, mkazi wa Hebere, adakatenga chikhomo cha hema, nakatenganso nyundo m'manja mwake, ndipo adayenda monyang'ama napita kwa Sisera uja. Pamene iyeyo anali m'tulo chifukwa chotopa, mkazi uja adakhomera chikhomo chija m'litsipa mwake. Chidatulukira kwinaku mpaka kuloŵa m'nthaka, iye kufa nkukhala komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yaele mkazi wa Hebere anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m'dzanja lake namdzera monyang'ama, nakhomera chichiri chilowe m'litsipa mwake; nichinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yaeli mkazi wa Heberi, anatenga chikhomo cha tenti ndi hamara ndi kupita mwakachetechete kwa Sisera uja. Tsono Sisera ali mtulo chifukwa chotopa, mkazi uja anamukhomera chikhomo chija mʼmutu mwake. Chinatulukira kwinaku mpaka kulowa mʼnthaka, ndipo anafa pomwepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yaeli mkazi wa Heberi anatenga ciciri ca hema, natenga nyundo m'dzanja lace namdzera monyang'ama, nakhomera ciciri cilowe m'litsipa mwace; nicinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa.