Judges 4:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Baraki adabwera akulondola Sisera, Yaele adatuluka kukamchingamira, namuuza kuti, “Loŵani, ndikuwonetseni munthu amene mukumfunayo.” Iye adaloŵa m'hema la mkaziyo, ndipo adangoona Sisera ali thasa pansi atafa, chikhomo cha hema chili tototo m'litsipa mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaele anatuluka kukomana naye, nati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo. Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m'litsipa mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Baraki atafika akulondola Sisera, Yaeli anatuluka kukamuchingamira namuwuza kuti, “Lowani mudzaone munthu amene mukumufunafuna.” Tsono atalowa anangoona Sisera ali thapsa pansi wakufa ndi chikhomo chili mʼmutu mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaeli anaturuka kukomana naye, Dati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo, Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi ciciri m'litsipa mwace.