Judges 4:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize, pakuti Sisera anali ndi magaleta achitsulo okwanira 900, ndipo adaazunza Aisraele mwankhalwe zaka makumi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli analira kwa Yehova kuti awathandize, chifukwa Sisera anali ndi magaleta achitsulo 900 ndipo anazunza Aisraeli mwankhanza kwa zaka makumi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova; pakuti anali nao magareta acitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israyeli kolimba zaka makumi awiri.