Judges 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Deborayo adatuma munthu kuti akaitane Baraki, mwana wa Abinowamu, wa ku Kedesi m'dziko la Nafutali. Baraki atabwera, Debora adamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akukulamula kuti, ‘Pita ukasonkhanitse anthu ako ku phiri la Tabori, ndipo utenge anthu 10,000 m'fuko la Nafutali ndi m'fuko la Zebuloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke m'Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Debora uja anatuma munthu kuti akayitane Baraki mwana wa Abinoamu wa ku Kedesi mʼdziko la Nafutali ndipo anati kwa iye, “Yehova Mulungu wa Israeli akukulamula iwe kuti, ‘Pita kasonkhanitse anthu ku phiri la Tabori. Ubwere nawo anthu 10,000 a fuko la Nafutali ndi a fuko la Zebuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinoamu, acoke m'Kedesi-Nafitali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nuluniike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni?