Judges 5:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku zitsime oimba akuimba nyimbo zokondwerera kuti Chauta wagonjetsa, zokondwerera kuti anthu ake ku Israele apambana.” “Tsono anthu a Chauta adasonkhana kuchokera ku midzi yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'milaga yake, m'Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta; kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana; akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli. “Choncho anthu a Yehova anasonkhana ku zipata za mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, Pomwepo adzafotokozera zolungama anazicita Yehova, Zolungama anazicita m'miraga yace, m'lsrayeli. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.