Judges 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakaloŵa m'chigwa kuchokera ku Efuremu, akukutsata iwe Benjamini, pamodzi ndi achibale ako. Kwa Makiri kudachokera atsogoleri a ankhondo, kwa Zebuloni kudachokera onyamula ndodo yaudindo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anafika Aefuremu amene adika mizu m'Amaleke; Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako. Ku Makiri kudachokera olamulira, ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu; akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako. Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri, ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anafika Aefraimu amene adika mizu m'Amaleki; Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako. Ku Makiri kudacokera olamulira, Ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.