Judges 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Olamulira a Isakara adabwera ndi Debora, anthu a kwa Isakara adatsatanso Baraki, nathamangira ku zigwa akumutsata. Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo, osadziŵa chenicheni choyenera kuchita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akalonga a Isakara anali ndi Debora; monga Isakara momwemo Baraki, anawatuma m'chigwa namka choyenda pansi. Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora; inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki, ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira. Koma pakati pa mafuko a Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akalonga a Isakara anali ndi Debora; Monga Isakara momwemo Baraki, Anawatuma m'cigwa namka coyenda pansi. Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikuru.