Judges 5:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani ankachedwa ku makola a nkhosa, kumangomvetsera zitoliro zoitanira nkhosa? Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo, osadziŵa chenicheni choyenera kuchita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wakhaliranji pakati pa makola, kumvera kulira kwa zoweta? Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera zitoliro zoyitanira nkhosa? Pakati pa anthu a fuko la Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wakhaliranji pakati pa makola, Kumvera kulira kwa zoweta? Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikuru.