Judges 5:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Agiliyadi adatsala patsidya pa Yordani. Nawonso anthu a kwa Dani, chifukwa chiyani ankachedwa m'zombo? Aasere ankangokhala m'madooko pa gombe la nyanja, ankangokhala m'madooko mwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Giliyadi anakhala tsidya lija la Yordani; ndi Dani, akhaliranji m'zombo? Asere anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja, nakhalitsa pa nyondo yake ya nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani. Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi? Aseri anali pa gombe la Nyanja; anangokhala mʼmadooko mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gileadi anakhala tsidya lija la Yordano; Ndi Dani, akhaliranji mzombo? Aseri anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja, Nakhalitsa pa nyondo yace ya nyanja.