Judges 5:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono ziboda za akavalo zidamveka kwambiri, akavalo ali paliŵiro, akuthamanga kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda. Ndi kutumphatumpha, kutumphatumpha kwa anthu ake eni mphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu, akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda, Ndi kutumphatumpha, kurumphatumpha kwa anthu ace eni mphamvu,