Judges 5:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenga chikhomo cha hema natenganso nyundo m'dzanja lake lamanja, adakhoma nacho Sisera, naphwanya mutu wake, adamutswanya ndi kumuboola m'litsipa mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dzanja lake analitambasulira kuchichiri, ndi dzanja lake lamanja ku nyundo ya antchito, nakhomera Sisera, nakantha mutu wake, inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake, anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja. Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake, ndi kumubowola mu litsipa mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dzanja lace analitambasulira kuciciri, Ndi dzanja lace lamanja ku nyundo ya anchito, Nakhomera Sisera, nakantha mutu wace, Inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwace.