Judges 5:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mai wake a Sisera adasuzumira pa zenera, nanena kuti, “Chifukwa chiyani galeta lake silikufika msanga? Bwanji mdidi wa akavalo a magaleta ake ukuchedwa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anapenyerera ali pazenera, nafuula Make wa Sisera, pa sefa wake, achedweranji galeta wake? Zizengerezeranji njinga za magaleta ake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera; nafuwula mokweza kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika? Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anapenyerera ali pazenera, napfuula Mace wa Sisera, pa made ace, Acedweranji gareta wace? Zizengerezeranji njinga za magareta ace?