Judges 5:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Kodi sakufunafuna zofunkha kuti agaŵane? Akugaŵira wankhondo aliyense mkazi mmodzi kapena aŵiri. Akugaŵira Sisera zofunkha, zovala zonyika mu utoto, zovala zopeta zonyika mu utoto, zovala ziŵiri zonyika mu utoto, zopeta kuti ndizivala m'khosi?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane; akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri. Sisera akumupatsa zofunkha: zovala zonyikidwa mu utoto, zoti ndizivala mʼkhosi zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi sanapeza, sanagawa zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu ali yense. Cofunkha ca nsaru za mawanga mawanga kwa Sisera; Cofunkha ca nsaru za mawanga mawanga, za maluwa, Nsaru za mawanga mawanga, za maluwa konse konse, kwa cofunkha ca khosi lace.