Judges 5:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene anthu adasankhula milungu ina, nkhondo idafika m'dziko. Mwa anthu 40,000 ku Israele, ndani adatenga chishango kapena mkondo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anasankha milungu yatsopano, pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata. Ngati chikopa kapena nthungo zidaoneka mwa zikwi makumi anai a Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene anasankha milungu ina, nkhondo inabwera ku zipata za mzinda, ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke pakati pa anthu 40,000 mu Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anasankha milungu yatsopano, Pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata. Ngati cikopa kapena nthungo zidaoneka Mwa zikwi makumi anai a Israyeli?